Politics

Mlembi wamkulu mchipani cha MCP apempha umodzi kuti chipanichi chipitirire kulamula mu chaka cha mawa


Wolemba: Linda Kwanjana

Mlembi wamkulu mchipani cha Malawi Congress (MCP) a Richard Chimwendo Banda lero  alengeza maina a wanthu omwe asankhidwa kukhala nawo mu komiti yaikulu yoyendetsa chipanichichi ya National Executive Committee (NEC).

Mkulankhula kwawo a Chimwendo Banda  apempha otsatira chipanichi kuti agwirane manja pomwe akugwirana manja ndi cholinga choti Chipani cha MCP chipitilire kulamula boma muchaka cha 2025.

A Banda anena kuti ndizosatheka kuti aliyese mchipani angakhale ndi mwayi okhala mu komitiyi.

A Chimwendo Banda anenetsa kuti chipanichi chinakhala pansi ndi kuunika modekha kuti anthu olimbikira okhawo ndiye awapatse mipando imeneyi.

Iwo anati , nthawi ya convetion idatha choncho iyi ndi nthawi yomanga chipani.

Nawo a Jesssie Kabwira omwe ndimneneli wachipanichi wanenetsa kuti komiti yasankhidwa ndi cholinga chofuna chipani cha MCP kuti chipitirire kulamula.

Ena omwe awasankha mipando ndi monga a Abida Mia omwe awasankha kukhala wachiwiri kwa wachiwiri wa mtsogoleri wachipanichi.

Tags

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close