Politics

MCP Convention: Ma delegates aku Lilongwe agwirizana kudzavotera Chithyola pampando wamlembi mchipani cha MCP

Olemba:  Mtolankhani wathu

Madelegates onse kuchokera kum’mawa wa Lilongwe komanso madera onse abomali lero amanga chimodzi cha mavu nkugwirizana kuti pa chisankho chikubwerachi chomwe chichitike mwezi wa August anthuwa adzabvotera
nduna ya Zachuma a Simplex Chithyola Banda yemwenso ndi phungu muboma la Kasungu.

Anthuwa alankhula izi lero pomwe a Chithyola adakumana ndi ma delegates a mzinda wa Lilongwe pamwambo omwe udachitikira ku likulu la chipanichi ku Lilongwe.

Chithyola Banda

Anthuwa awuza ndunayi kuti munthawi yochepa yomwe a Chithyola akhala akuyenda kumema anthu , awonetsa mtima odzichepetsa komanso opanda tsankho.

Mukulankhula kwawo a Chithyola adati nthawi yakwana kuti iwo atenge mpando wa ukulu onga uwu chifukwa ali ndi chikhulupiliro kuti abweretsa kusintha kwakukulu mu chipanichi.

Tags

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close